Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 46:25-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Amenewa ndi ana a Biliha, amene Labani anampatsa Rakele mwana wace wamkazi, amenewo anambalira Yakobo; anthu onse ndiwo asanu ndi awiri.

26. Ndi anthu onse amene anadza ndi Yakobo m'Aigupto, amene anaturuka m'cuuno mwace, pamodzi ndi akazi a ana amuna a Yakobo ndiwo makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi mmodzi;

27. ndi ana amuna a Yosefe, amene anambadwira iye m'Aigupto ndiwo anthu awiri; anthu onse a mbumba ya Yakobo, amene analowa m'Aigupto anali makumi asanu ndi awiri.

28. Ndipo anatumiza Yuda patsogolo pace kwa Yosefe, amtsogolere kumuonetsa njira yomka ku Goseni: ndipo anafika ku dziko la Goseni.

29. Ndipo Yosefe anamanga gareta lace nakwera kunka kukakomana naye Israyeli atate wace, ku Goseni, ndipo anadzionetsera yekha kwa iye, nagwera pakhosi pace nakhala m'kulira pakhosi pace.

30. Ndipo Israyeli anati kwa Yosefe, Ndife tsopano, popeza ndaona nkhope yako, kuti ukali ndi moyo.

31. Ndipo Yosefe anati kwa abale ace, ndi kwa mbumba ya atate wace, Ndidzanka, ndikauze Farao, ndipo ndidzati kwa iye, Abale anga ndi mbumba ya atate wanga, amene anali m'dziko la Kanani, afika kwa ine;

32. ndipo anthuwo ali abusa cifukwa anakhala oweta ng'ombe; ndipo anadza ndi nkhosa zao ndi ng'ombe zao ndi zonse ali nazo.

33. Ndipo padzakhala pamene Farao adzaitana inu, nadzati, Nchito yanu njotani?

34. mudzati, Akapolo anu akhala oweta ng'ombe ciyambire ubwana wathu kufikira tsopano, ife ndi atate athu; kuti mukhale m'dziko la Goseni; a cifukwa abusa onse anyansira Aaigupto.

Werengani mutu wathunthu Genesis 46