Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 46:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Israyeli anamuka ulendo wace ndi zonse anali nazo, nafika ku Beereseba, napereka nsembe kwa Mulungu wa Isake atate wace.

2. Ndipo Mulungu ananena kwa Israyeli, m'masomphenya a usiku, nati, Yakobo, Yakobo.

3. Nati iye, Ndine pano. Ndipo anati, Ine ndine Mulungu, Mulungu wa atate wako; usaope kunka ku Aigupto; pakuti pamenepo ndidzakusandutsa iwe mtundu waukuru;

4. Ine ndidzatsikira pamodzi ndi iwe ku Aigupto; ndipo Ine ndidzakubwezanso ndithu; ndipo Yosefe adzaika dzanja lace pamaso pako.

5. Ndipo Yakobo anacoka ku Beereseba, ndipo ana amuna a Israyeli anamnyamula Yakobo atate wao, ndi ana ao ang'ono, ndi akazi ao, m'magareta amene Farao anatumiza kuti amnyamule iye,

6. Ndipo anatenga ng'ombe zao ndi cuma cao anacipezam'dziko la Kanani, nadza ku Aigupto, Yakobo ndi mbeu zace zonse pamodzi ndi iye;

7. ana ace amuna, ndi zidzukulu zace zazimuna, ndi ana akazi ace, ndi zidzukulu zace zazikazi, ndi mbeu zace zonse anadza nazo m'Aigupto.

8. Maina a ana a Israyeli amene anadza m'Aigupto ndi awa: Yakobo ndi ana amuna ace: Rubeni mwana wamwamuna woyamba wa Yakobo.

Werengani mutu wathunthu Genesis 46