Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 44:9-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. iye wa akapolo anu ampeza naco afe, ndipo ifenso tidzakhala akapolo a mbuyanga.

10. Ndipo iye mati, Tsononso cikhale monga mwa nau anu: iye amene ampeza naco adzakhala kapolo wanga; ndipo inu nudzakhala opanda cifukwa.

11. Ndipo anafulumira natsitsa pansi zense thumba lace, namasula yense humba lace.

12. Ndipo iye anafunauna kuyambira pa wamkuru naleka pa wamng'ono; nacipeza cikho n'thumba la Benjamini:

13. ndipo anang'amba zobvala zao, nasenzetsa yense buru wace, nabwera kumuzi.

14. Yudanso ndi abale ace anadza cu nyumba ya Yosefe; ndipo iye ikali pamenepo; ndipo anagwa oansi patsogolo pace.

15. Ndipo losefe anati kwa iwo, Ici nciani nwacicita? Kodi simudziwa kuti nunthu ngati ine ndingathe kuzindidra ndithu?

16. Ndico Yuda anati, Kodi tidzati bwanji kwa mbuyanga? kodi tidzanenanji? kapena tidzawiringula ife bwanji? Mulungu wapeza mphulupulu ya akapolo anu; taonani, tiri akapolo a mbuyanga, ife ndi iye amene anampeza naco cikho m'dzanja lace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 44