Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 44:20-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndipo tinati kwa mbuyanga, Tiri ndi atate, munthu wokalamba, ndi mwana wa ukalamba wace wamng'ono; mbale wace wafa, ndipo iye yekha watsala wa amace, ndipo atate wace amkonda iye.

21. Ndipo munati kwa akapolo anu, Munditengere iye, kuti ndimuone iye m'maso mwanga.

22. Ndipo ife tinati kwa mbuyanga, Mnyamata sangathei kumsiya atate wace; pakuti akamsiya atate wace, atate wace adzafa.

23. Ndipo munati kwa akapolo anu, Koma ngati mbale wanu safika pamodzi ndi inu, simudzaonanso konse nkhope yanga,

24. Ndipo panali titakwera kunka kwa kapolo wanus atate, wanga, tinamfotokozera iye mau a mbuyanga.

25. Ndipo atate wathu anati, Mupitenso mutigulire ife cakudya pang'ono.

26. Ndipo ife tinati, Sitingathe kupita; mphwathu wamng'ono akakhala ndi ife, pamenepo tidzapita; pakuti sitingaone nkhope ya munthu uja, mphwathu wamng'ono akapanda kukhala ndi ife.

27. Ndipo kapolo wanu atate wanga anati kwa ife, Inu mudziwa kuti mkazi wanga anandibalira ine ana amuna awiri;

28. wina anaturuka kwa ine ndipo ndinati, Zoonatu, wakadzulidwa; ndipo sindidzamuonanso iye;

29. ndipo ngati mukandicotsera ameneyonso, ndipo ngati cimgwera coipa, mudzanditsitsira ndi cisoni imvi zanga kumanda.

30. Cifukwa cace ndikafika kwa kapolo wanu atate wanga, ndipo mnyamata akapanda kukhala ndi ife; popeza moyo wace uli womangidwa ndi moyo wa mnyamatayo;

31. kudzakhala pakuona kuti mnyamatayo palibe, adzafa; ndipo akapolo anu adzamtsitsira ndi cisoni imvi za atate wathu kumanda.

32. Pakuti kapolo wanu anadziyesa cikole ca mnyamata pa atate wanga, kuti, Ndikapanda kumbwezeranso kwa inu, pamenepo ndidzakhala ndi cifukwa kwa atate wanga nthawi zonse.

33. Tsopanotu, mtumiki wanu akhale kapolo wa mbuyanga m'malo mwa mnyamata; mnyamatayo akwere pamodzi ndi abale ace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 44