Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 44:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yosefe anauza tsanyumba wace kuti, Dzaza matumba a anthuwo ndi cakudya, monga angathe kunyamula, ndi kuika ndalama za yense kukamwa kwa thumba lace.

2. Nuike cikho canga, cikho casiliva ciija, kukamwa kwa thumba la wamng'ono, pamodzi ndi ndalama za tirigu zace. Ndipo iye anacita monga mau ananena Yosefe.

3. Pamene kudaca, anamukitsa anthu iwo ndi aburu ao.

4. Ataturuka m'mudzi asanamuke patari, Yosefe anati kwa tsanyumba wace, Tanyamuka, talondola anthu aja, ukawapeza unene nao, Cifukwa canji mwabwezera zoipa m'malo mwa zabwino?

5. Kodi si ndico comwera naco mbuyanga, naombeza ula naco? Mwacitira coipa pakutero.

6. Ndipo anapeza iwo, nanena nao mau omwewo.

7. Nati kwa iye, Bwanji mbuyanga anena mau otere? Ngati nkutheka kuti akapolo anu acite cotero?

8. Taonani, ndalama zija, tinazipeza kukamwa kwa matumba athu, tinazibwezanso kwa inu kuturuka m'dziko la Kanani; nanga bwanji tingabe m'nyumba ya mbuyanga kapena siliva kapena golidi?

9. iye wa akapolo anu ampeza naco afe, ndipo ifenso tidzakhala akapolo a mbuyanga.

10. Ndipo iye mati, Tsononso cikhale monga mwa nau anu: iye amene ampeza naco adzakhala kapolo wanga; ndipo inu nudzakhala opanda cifukwa.

11. Ndipo anafulumira natsitsa pansi zense thumba lace, namasula yense humba lace.

12. Ndipo iye anafunauna kuyambira pa wamkuru naleka pa wamng'ono; nacipeza cikho n'thumba la Benjamini:

Werengani mutu wathunthu Genesis 44