Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 43:28-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Ndipo iwo anati, Kapolo wanu atate wathu ili bwino, alipo. Ndipo anawerama, namgwadira iye.

29. Ndipo iye anatucula maso ace naona Benjamini mphwace, mwana wa amace, nati, Kodi uyu ndi mphwanu wamng'ono uja, amene munanena ndi ine uja? Ndipo iye anati, Mulungu akucitire we ufulu, mwana wanga.

30. Ndipo Yosefe anafulumira, cifukwa mtima wace unakhumbitsa mphwace, ndipo mafuna polirira; nalowa m'cipinda ace naliramo.

Werengani mutu wathunthu Genesis 43