Ndipo Yosefe anaona abale ace, ndipo anazindikira iwo, koma anadziyesetsa kwa iwo ngati mlendo, nanena kwa iwo mwankhanza: ndipo anati kwa iwo, Mufuma kuti inu? nati iwo, Ku dziko la Kanani kudzagula cakudya.