Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 42:5-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo ana amuna a Israyeli anadza kudzagula mwa iwo amene anadzako, pakuti m'dziko la Kanani munali njala.

6. Ndipo Yosefe anali wolamulira dziko; ndiye amene anagulitsa kwa anthu onse a m'dziko; ndipo anafika abale ace a Yosefe, namweramira pansi, nkhope zao pansi.

7. Ndipo Yosefe anaona abale ace, ndipo anazindikira iwo, koma anadziyesetsa kwa iwo ngati mlendo, nanena kwa iwo mwankhanza: ndipo anati kwa iwo, Mufuma kuti inu? nati iwo, Ku dziko la Kanani kudzagula cakudya.

8. Ndipo Yosefe anazindikira abale ace, koma iwo sanamzindikira iye.

9. Ndipo Yosefe anakumbukira maloto amene analoto za iwo, ndipo anati kwa iwo, Ozonda inu; mwadzera kudzaona usiwa wa dziko.

10. Ndipo iwo anati kwa iye, Iai, mbuyanga, koma akapolo anu adzera kudzagula cakudya.

11. Tonse tiri ana amuna a munthu mmodzi; tiri oona, akapolo anu, sitiri ozonda.

12. Ndipo iye anati kwa iwo, Iai, koma mwadzera kuti muone usiwa wa dziko.

13. Nati iwo, Akapolo anu ndife abale khumi, ana amuna a munthu mmodzi m'dziko la Kanani; ndipo, taonani, wamng'ono ali ndi atate wathu lero; ndipo palibe mmodzi.

14. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, dico cimene ndinakunenani inu, kuti, Ndinu ozonda.

15. Mudzayesedwa ndi ici, pali moyo wa Farao, simudzaturuka muno, koma akadze kuno mphwanu ndiko.

16. Tumizani mmodzi wa inu akatenge, adze naye mphwanu: ndipo inu mudzamangidwa kuti mau anu ayesedwe, ngati zoona ziri mwa inu: penatu, pali moyo wa Farao, muli ozonda ndithu.

17. Ndipo anaika onse m'kaidi masiku atatu.

18. Ndipo Yosefe anati kwa iwo tsiku lacitatu, Citani ici, kuti mukhale ndi moyo; ine ndiopa Mulungu;

Werengani mutu wathunthu Genesis 42