Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 42:10-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo iwo anati kwa iye, Iai, mbuyanga, koma akapolo anu adzera kudzagula cakudya.

11. Tonse tiri ana amuna a munthu mmodzi; tiri oona, akapolo anu, sitiri ozonda.

12. Ndipo iye anati kwa iwo, Iai, koma mwadzera kuti muone usiwa wa dziko.

13. Nati iwo, Akapolo anu ndife abale khumi, ana amuna a munthu mmodzi m'dziko la Kanani; ndipo, taonani, wamng'ono ali ndi atate wathu lero; ndipo palibe mmodzi.

14. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, dico cimene ndinakunenani inu, kuti, Ndinu ozonda.

15. Mudzayesedwa ndi ici, pali moyo wa Farao, simudzaturuka muno, koma akadze kuno mphwanu ndiko.

16. Tumizani mmodzi wa inu akatenge, adze naye mphwanu: ndipo inu mudzamangidwa kuti mau anu ayesedwe, ngati zoona ziri mwa inu: penatu, pali moyo wa Farao, muli ozonda ndithu.

17. Ndipo anaika onse m'kaidi masiku atatu.

18. Ndipo Yosefe anati kwa iwo tsiku lacitatu, Citani ici, kuti mukhale ndi moyo; ine ndiopa Mulungu;

19. ngati muli oona, mmodzi wa abale anu amangidwe m'kaidi momwemo; mukani inu, mupite naye tirigu wa njala ya mabanja anu;

20. koma mukatenge mphwanu kudza naye kwa ine, kuti atsimikizidwe mau anu ndipo simudzafa. Ndipo anacita comweco.

21. Ndipo iwo anati wina ndi mnzace, Tacimwiratu mbale wathu, pamene tinaona kubvutidwa kwa mtima wace, potipembedzera ife, koma ife tinakana kumvera, cifukwa cace kubvutidwa kumene kwatifikira.

22. Ndipo Rubeni anayankha nati kwa iwo, Kodi sindinanena kwa inu kuti, Musacimwire mwanayu; ndipo inu munakana kumvera? cifukwa cacenso, taonani mwazi wace ufunidwa.

23. Ndipo sanadziwa kuti, Yosefe anamva; cifukwa anali ndi womasulira.

24. Ndipo anawafotokozera iwo nalira, nawatembenukiranso, nanena nao, nampatula Simeoni mwa iwo, nammanga iye pamaso pao.

25. Ndipo Yosefe analamulira kuti adzaze zotengera zao ndi tirigu, ndi kubweza ndalama zao, ali yense m'thumba mwace, ndi kuwapatsa phoso la panjira; ndipo anatero nao.

Werengani mutu wathunthu Genesis 42