1. Ndipo anaona Yakobo kuti m'Aigupto munali tirigu, nati Yakobo kwa ana ace amuna, Cifukwa canji mulinkuyang'anana?
2. Ndipo iye anati, Taonani, ndamva kuti m'Aigupto muli tirigu, mutsikireko mutigulire kumeneko; kuti tikhale ndi moyo, tisafe.
3. Ndipo abale ace a Yosefe khumi anatsikira kukagula tirigu m'Aigupto.
4. Koma Yakobo sanamtuma Benjamini mphwace wa Yosefe, pamodzi ndi abale ace, cifukwa anati, Coipa cingamgwere iye.
5. Ndipo ana amuna a Israyeli anadza kudzagula mwa iwo amene anadzako, pakuti m'dziko la Kanani munali njala.
6. Ndipo Yosefe anali wolamulira dziko; ndiye amene anagulitsa kwa anthu onse a m'dziko; ndipo anafika abale ace a Yosefe, namweramira pansi, nkhope zao pansi.
7. Ndipo Yosefe anaona abale ace, ndipo anazindikira iwo, koma anadziyesetsa kwa iwo ngati mlendo, nanena kwa iwo mwankhanza: ndipo anati kwa iwo, Mufuma kuti inu? nati iwo, Ku dziko la Kanani kudzagula cakudya.