Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 41:28-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Ici ndi cinthu cimene ndinena kwa Farao: cimene Mulungu ati acite wasonyeza kwa Farao.

29. Taonani, zidzafika zaka zisanu ndi ziwiri zakucuruka cakudya m'dziko lonse la Aigupto;

30. ndipo pambuyo pao zidzauka zaka zisanu ndi ziwiri za njala; ndipo anthu adzaiwala zocuruka zonsezo m'dziko la Aigupto; ndipo njala idzapululutsa dziko;

31. ndipo zocuruka sizidzazindikirika cifukwa ca njala ikudza m'mbuyoyo, pakuti idzabvuta.

32. Ndipo lotolo linabwezedwa kawiri kwa Farao, cifukwa cinthu ciri cokhazikika ndi Mulungu, ndipo Mulungu afulumira kucicita.

33. Tsopano, Farao afunefune'munthu wakuzindikira ndi wanzeru, amkhazike iye ayang'anire dziko la Aigupto.

34. Farao acite cotere, alembe woyang'anira dziko wosonkhetsa limodzi la magawo asanu la dziko la Aigupto m'zaka zisanu ndi ziwiri zakucuruka dzinthu.

35. Iwo asonkhanitse cakudya conse ca zaka zabwino izo zirinkudzazo, aunjike tirigu m'manja a Farao akhale cakudya m'midzi, namsunge.

Werengani mutu wathunthu Genesis 41