Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 41:27-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zoonda ndi za maonekedwe oipa zinaturuka pambuyo pao ndizo zaka zisanu ndi ziwiri, ndiponso ngala zisanu ndi ziwiri zopanda kanthu zopsyerera ndi mphepo ya kum'mawa, ndizo zaka zisanu ndi ziwiri za njala.

28. Ici ndi cinthu cimene ndinena kwa Farao: cimene Mulungu ati acite wasonyeza kwa Farao.

29. Taonani, zidzafika zaka zisanu ndi ziwiri zakucuruka cakudya m'dziko lonse la Aigupto;

30. ndipo pambuyo pao zidzauka zaka zisanu ndi ziwiri za njala; ndipo anthu adzaiwala zocuruka zonsezo m'dziko la Aigupto; ndipo njala idzapululutsa dziko;

31. ndipo zocuruka sizidzazindikirika cifukwa ca njala ikudza m'mbuyoyo, pakuti idzabvuta.

32. Ndipo lotolo linabwezedwa kawiri kwa Farao, cifukwa cinthu ciri cokhazikika ndi Mulungu, ndipo Mulungu afulumira kucicita.

Werengani mutu wathunthu Genesis 41