Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 41:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo panali zitapita zaka ziwiri zamphumphu, Farao analota; ndipo, taonani, anaima panyanja.

2. Ndipo, taonani, zinaturuka m'nyanja ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe okoma ndi zonenepa; ndipo zinadya mabango.

3. Ndipo, taonani ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zinaturuka m'nyanjamo pambuyo pao, za maonekedwe oipa ndi zoonda; ndipo zinaima pa ng'ombe zinazo m'mphepete mwa nyanja.

4. Ndipo ng'ombe zazikazi za maonekedwe oipa ndi zoonda zinadya ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe abwino ndi zonenepazo. Ndipo Farao anauka.

5. Ndipo anagona nalotanso kaciwiri: ndipo taonani, ngala zisanu ndi ziwiri za tirigu zinamera pa mbuwa imodzi, zonenepa ndi zabwino.

6. Ndipo, taonani, ngala zisanu ndi ziwiri, zoonda zopsyerera ndi mphepo ya kum'mawa, zinamera pambuyo pao.

7. Ndipo ngala zoondazo zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zonenepa ndi zodzalazo. Ndipo Farao anauka, ndipo, taonani, analota.

8. Ndipo panali m'mamawa mtima wace unabvutidwa; ndipo anatumiza naitana amatsenga onse a m'Aigupto, ndi anzeru onse a momwemo: ndipo Farao anafotokozera iwo loto lace; koma panalibe mmodzi anakhoza kuwamasulira iwo kwa Farao.

9. Pamenepo wopereka cikho wamkuru anati kwa Farao, kuti, Ine ndidzakumbukira zocimwa zanga lero.

10. Farao anakwiya ndi anyamata ace, nandiika ine ndisungidwe m'nyumba ya kazembe wa alonda, ine ndi wophika mkate wamkuru:

Werengani mutu wathunthu Genesis 41