Ndiponso kwa Seti, kwa iye kunabadwamwana wamwamuna: anamucha dzina lace Enosi: pomwepo anthu anayamba kuchula dzina la Yehova.