Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 39:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anatsika naye Yosefe kunka ku Aigupto; ndipo Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda, Maigupto, anamgula iye m'manja mwa Aismayeli amene anatsika naye kunka iumeneko.

2. Ndipo Yehova anali ndi Yosefe; ndipo iye anali wolemeralemera; nakhala m'nyumba ya mbuyace M-aigupto.

3. Ndipo mbuyace anaona kuti Yehova anali ndi iye, ndi kuti Yehova anamlemereza m'dzanja lace zonse anazicita.

4. Ndipo Yosefe anapeza ufulu pamaso pace, ndipo anamtumikira iye; ndipo anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yace, naika m'manja mwace zonse anali nazo.

Werengani mutu wathunthu Genesis 39