Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 34:27-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ndipo ana amuna a Yakobo anadzakwa ophedwa nafunkhamudzi cifukwa anamuipitsa mlongo wao.

28. Ndipo analanda nkhosa zao ndi zoweta zao ndi aburu ao, ndi za m'mudzi, ndi za m'munda;

29. ndi cuma cao conse ndi ana ao ndi akazi ao anawagwira, nafunkha zonse za m'nyumba.

30. Ndipo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, Mwaodisautsa ndi kundinunkhitsa ine mwa anthu okhala m'dzikomu, mwa Akanani ndi mwa Aperezi; ndipo ine ndine wa anthu owerengeka, adzandisonkhanira ine ndi kundikantha: ndipo ndidzapasulidwa ine ndi a pa nyumba yanga.

31. Ndipo iwo anati, Kodi iye ayenera kusandutsamloogo wathu wadama?

Werengani mutu wathunthu Genesis 34