Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 34:19-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo mnyamatayo sanacedwa kucicita popeza anakondwera ndi mwana wace wamkazi wa Yakobo; ndipo iye anali wolemekezedwa woposa onse a pa banja la atate wace.

20. Ndipo Hamori ndi Sekemu mwana wace anafika ku cipata ca mudzi wao, nalankhulana ndi anthu a mudzi wao, kuti,

21. Anthu amenewa ali amtendere pamodzi ndi ife; cifukwa cace akhale m'dzikomo, acite malonda m'menemo: pakuti taonani dzikololirilalikurulokwaniraiwo; tidzitengere ana ao akazi akhale akazi athu, tiwapatse amenewa ana athu akazi.

22. Anthuwo adzatiloleza ife tikhale nao anthu amodzi, pokhapo amuna onse a mwa ife adzadulidwa, monga iwo adulidwa.

23. Kodi ng'ombe zao ndi cuma cao ndi zoweta zao sizidzakhala zathu? Pokhapo tibvomerezana nao ndipo adzakhala pamodzi ndi ife.

24. Ndipo onse amene anaturuka pa cipata ca mudzi wao anamvera Hamori ndi mwana wace Sekemu, nadulidwa amuna onse akuturuka pa cipata ca mudzi wao.

25. Ndipo panali tsiku lacitatu pamene anamva kuwawa, ana amuna awiri a Yakobo, Simeoni ndi Levi, abale ace a Dina, anatenga wina lupanga lace wina lace, nalimbika mtima nalowa m'mudzi napha amuna onse.

26. Ndipo anapha Hamori ndi Sekemu mwana wace ndi lupanga, naturutsa Dina m'nyumba ya Sekemu nacoka naye.

27. Ndipo ana amuna a Yakobo anadzakwa ophedwa nafunkhamudzi cifukwa anamuipitsa mlongo wao.

28. Ndipo analanda nkhosa zao ndi zoweta zao ndi aburu ao, ndi za m'mudzi, ndi za m'munda;

Werengani mutu wathunthu Genesis 34