Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 33:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yakobo anatukula maso ace, taonani, anadza Esau, ndi pamodzi naye anthu mazana anai. Ndipo anagawira ana kwa Leya, ndi kwa Rakele, ndi kwa adzakazi awiri aja.

2. Ndipo anaika adzakazi ndi ana ao patsogolo, ndi Leya ndi ana ace pambuyo pao, ndi Rakele ndi Yosefe pambuyo pa onse.

3. Ndipo iye mwini anatsogolera patsogolo pao, nawerama pansi kasanu ndi kawiri mpaka anayandikira mkuru wace.

4. Ndipo Esau anathamangira kukomana naye namfungatira, nagwa pankhope pace, nampsompsona; ndipo analira iwo.

5. Ndipo anatukula maso ace nawaona akazi ndi ana; nati, Ndani awa ali ndi iwe? Ndipo iye anati, Ndiwo ana amene Mulungu anakomera mtima kumpatsa kapolo wanu.

6. Ndipo adzakazi anayandikira ndi ana ao, nawerama pansi.

7. Ndiponso Leya ndi ana ace anayandikira nawerama pansi: pambuyo pace anayandikira Yosefe ndi Rakele, nawerama pansi,

8. Ndipo anati, Nanga khamu lonse limene ndinakomana nalo nlotani? Ndipo anati, Kuti ndipeze ufulu pamaso pa mbuyanga.

9. Ndipo Esau anati, Zanga zindifikira; mbale wanga, khala nazo zako iwe wekha.

10. Ndipo! Yakobo anati, Iaitu, ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, mulandire mphatso yanga pa dzanja langa; pakuti popeza ndinaona nkhope yanu, monga anthu aona nkhope ya Mulungu, ndipo inu mwanelibvomereza ine.

11. Landiranitu mdalitso wanga umene wafika kwa inu, pakuti Mulungu wandicitira ine zaufulu, ndipo zanganso zindifikira. Ndipo anamkakamiza, nalandira.

12. Ndipo Esau anati, Tiyeni timuke; nditsogolera ndine.

13. Ndipo anati kwa iye, Mbuyanga adziwa kuti ana ali ambowa, ndipo nkhosa ndi zoweta ndiri nazo zirinkuyamwitsa: ndipo akathamangitsa tsiku limodzi zoweta zonse zidzafa.

Werengani mutu wathunthu Genesis 33