Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 31:45-55 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

45. Ndipo Yakobo anatenga mwala, nauimiritsa.

46. Ndipo Yakobo anati kwa abale ace, Sonkhanitsani miyala; ndipo anasonkhanitsa miyala nakundika mulu: ndipo anadya pamulupo.

47. Ndipo Labani anacha pamenepo Yegara-sahaduta; koma Yakobo anacha Galeeda.

48. Ndipo Labani anati, Muluwu ndiwo mboni pakati pa ine ndi iwe lero. Cifukwa cace anacha dzina lace, Galeeda;

49. ndi Mizipa, cifukwa kuti anati, Yehova ayang'anire pakati pa ine ndi iwe, pamene tisiyana wina ndi mnzace.

50. Ukasautsa ana anga akazi, kapena ukatenga akazi kuonjezera pa ana anga, palibe munthu mmodzi ali nafe; taonani, Mulungu ndiye mboni yanga ndi yako.

51. Ndipo Labani anati kwa Yakobo. Taona muluwu, taona coimiritsaci, ndaciimiritsa pakati pathu.

52. Muluwu ndiwo mboni, coimiritsaci ndico mboni, kuti ine sindidzapitirira pa muluwu kunka kwa iwe, ndipo iwe sudzapitirira pa muluwu ndi pa coimiritsaci kudza kwa ine kuti ticitirane zoipa,

53. Mulungu wa Abrahamu ndi Mulungu wa Nahori, Mulungu wa atate wao aweruze pa ife. Ndipo Yakobo analumbirira pa Kuopsa kwa atate wace Isake.

54. Ndipo Yakobo anapereka nsembe paphiripo, naitana abale ace kuti adye cakudya; ndipo anadya cakudya, nagona paphiripo usiku wonse.

55. M'mamawa Labani anauka nampsompsona ana ace amuna ndi akazi, nawadalitsa: ndipo Labani anacoka, nabwera kumalo kwace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 31