Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 31:10-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo panali potenga mabere ziwetozo, ine ndinatukula maso anga, ndipo ndinapenya m'kulota, taonani, atonde okwera ziweto anali amipyololo-mipyololo, amathotho-mathotho, ndi amaanga-maanga.

11. Mthenga wa Mulungu ndipo anati kwa ine m'kulotamo, Yakobo; nati ine, Ndine pano,

12. Ndipo anati, Tukulatu maso ako, nuone, atonde onse amene akwera zoweta ali amipyololo-mipyololo, amathotho-mathotho, ndi amaangamaanga: cifukwa ndaona zonse zimene Labani akucitira iwe.

13. Ine ndine Mulungu wa ku Beteli, kuja unathira mafuta pamwala paja, pamene unandilumbirira ine cilumbiriro: tsopano uka, nucoke m'dziko lino, nubwerere ku dziko la abale ako.

14. Ndipo Rakele ndi Leya anayankha, nati kwa iye, Kodi tiri nalonso gawo kapena colowa m'nyumba ya atate wathu?

15. Kodi satiyesa ife alendo? cifukwa anatigulitsa ife, nathanso kuononga ndalama zathu.

16. Cifukwa kuti cuma conse Mulungu anacicotsa kwa atate wathu ndi cathu ndi ca ana athu; tsono, zonse wakunenera iwe Mulungu, ucite.

17. Ndipo anauka Yakobo nakweza ana ace ndi akazi ace pa ngamila;

18. ndipo ananka nazo zoweta zace zonse, ndi cuma cace conse anacisonkhanitsa, zoweta zace anaziona m'Padan-aramu, kuti anke kwa Isake atate wace ku dziko la Kanani.

19. Ndipo Labani ananka kukasenga nkhosa zace: ndipo Rakele anaba aterafi a atate wace.

20. Ndipo Yakobo anathawa kwa Labani Msuriyamobisika, m'mene sanamuuzeiye kuti analinkuthawa.

Werengani mutu wathunthu Genesis 31