Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 3:6-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m'maso, mtengo wolakalakika wakupatsa nzeru, anatenga zipatso zace, nadya, napatsanso mwamuna wace amene ali nave, nadya iyenso,

7. Ndipo anatseguka maso ao a onse awiri, nadziwa kuti anali amarisece: ndipo adasoka masamba amkuyu, nadzipangira mateweta.

8. Ndipo anamva mau a Yehova Mulungu alinkuyendayenda m'munda nthawi yamadzulo: ndipo anabisala Adamu ndi mkazi wace pamaso pa Yehova Mulungu pakati pa mitengo ya m'munda.

9. Ndipo Yehova Mulungu anaitana mwamunayo nati kwa iye, Uli kuti?

10. Ndipo anati, Ndinamva mau anu m'mundamu, ndipo ndinaopa cifukwa ndinali wamarisece ine; ndipo ndinabisala.

11. Ndipo anati, Ndani anakuuza iwe kuti uli wamarisece? Kodi wadya za mtengo uja, umene ndinakuuza iwe kuti usadye?

12. Ndipo anati mwamunayo, Mkazi amene munandipatsa ine kuti akhale ndi ine, ameneyo anandipatsa ine za mtengo, ndipo ndinadya.

13. Ndipo Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, Ciani cimene wacitaci? Ndipo anati mkaziyo, Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.

14. Ndipo anati Yehova Mulungu kwa njokayo, Cifukwa kuti wacita ici, wotembereredwa ndiwe wopambana ndi zinyama zonse ndi zamoyo zonse za m'thengo: uziyenda ndi pamimba pako, uzidya pfumbi masiku onse a moyo wako:

15. ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yace; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira citende cace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 3