Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 3:4-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Njokayo ndipo inati kwa mkaziyo, Kufa simudzafai;

5. cifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.

6. Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m'maso, mtengo wolakalakika wakupatsa nzeru, anatenga zipatso zace, nadya, napatsanso mwamuna wace amene ali nave, nadya iyenso,

7. Ndipo anatseguka maso ao a onse awiri, nadziwa kuti anali amarisece: ndipo adasoka masamba amkuyu, nadzipangira mateweta.

8. Ndipo anamva mau a Yehova Mulungu alinkuyendayenda m'munda nthawi yamadzulo: ndipo anabisala Adamu ndi mkazi wace pamaso pa Yehova Mulungu pakati pa mitengo ya m'munda.

9. Ndipo Yehova Mulungu anaitana mwamunayo nati kwa iye, Uli kuti?

10. Ndipo anati, Ndinamva mau anu m'mundamu, ndipo ndinaopa cifukwa ndinali wamarisece ine; ndipo ndinabisala.

11. Ndipo anati, Ndani anakuuza iwe kuti uli wamarisece? Kodi wadya za mtengo uja, umene ndinakuuza iwe kuti usadye?

Werengani mutu wathunthu Genesis 3