Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 3:19-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. m'thukuta la nkhope yako udzadya cakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: cifukwa kuti m'menemo unatengedwa: cifukwa kuti ndiwe pfumbi, ndi kupfumbiko udzabwerera.

20. Ndipo mwamuna anamucha dzina la mkazi wace, Hava; cifukwa ndiye amace wa amoyo onse.

21. Yehova Mulungu ndipo anapangira Adamu ndi mkazi wace maraya azikopa, nawabveka iwo.

22. Ndipo anati Yehova Mulungu, Taonani, munthuyo akhala ngati mmodzi wa ife, wakudziwa zabwino ndi zoipa: ndipo tsopano kuti asatambasule dzanja lace ndi kutenga za mtengo wa moyo, ndi kudya, ndi kukhala ndi moyo nthawi zonse,

23. Yehova Mulungu anamturutsa iye m'munda wa Edene, kuti alime nthaka m'mene anamtenga iye.

24. Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazika Makerubi ca kum'mawa kwace kwa munda wa Edene, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.

Werengani mutu wathunthu Genesis 3