Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 3:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo njoka inali yakucenjera yoposa zamoyo zonse za m'thengo zimene anazipanga Yehova Mulungu, Ndipo inati kwa mkaziyo, Ea! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m'mundamu?

2. Mkaziyo ndipo anati kwa njoka, Zipatso za mitengo ya m'mundamu tidye.

3. Koma zipatso za mtengo umene uti m'kati mwa munda, Mulungu anati, Musadye umenewo, musakhudze umenewo, mungadzafe.

4. Njokayo ndipo inati kwa mkaziyo, Kufa simudzafai;

5. cifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.

6. Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m'maso, mtengo wolakalakika wakupatsa nzeru, anatenga zipatso zace, nadya, napatsanso mwamuna wace amene ali nave, nadya iyenso,

7. Ndipo anatseguka maso ao a onse awiri, nadziwa kuti anali amarisece: ndipo adasoka masamba amkuyu, nadzipangira mateweta.

8. Ndipo anamva mau a Yehova Mulungu alinkuyendayenda m'munda nthawi yamadzulo: ndipo anabisala Adamu ndi mkazi wace pamaso pa Yehova Mulungu pakati pa mitengo ya m'munda.

9. Ndipo Yehova Mulungu anaitana mwamunayo nati kwa iye, Uli kuti?

10. Ndipo anati, Ndinamva mau anu m'mundamu, ndipo ndinaopa cifukwa ndinali wamarisece ine; ndipo ndinabisala.

Werengani mutu wathunthu Genesis 3