Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 27:11-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Yakobo ndipo anati kwa Rebeka amace, Taonani, Esau mkuru wanga ndiye munthu waubweya, ine ndine munthu, wosalala.

12. Kapena atate wanga adzandiyambasa, ndipo ndidzaoneka pamaso pace ngati wakunyenga; pamenepo ndidzadzitengera ine temberero, si mdalitso.

13. Ndipo amace anati kwa iye, Pa ine likhale temberero lako mwana wanga; koma tamvera mau anga, kazimuka kunditengera timeneto.

14. Ndipo anamuka nakatenga nadza nato kwa amace; amace ndipo anakonza cakudya cokolera conga cimene anacikonda atate wace.

15. Ndipo Rebeka anatenga zobvala zokoma za Esau, mwana wace wamkuru zinali m'nyumba, nabveka nazo Yakobo mwana wace wamng'ono;

16. ndipo anabveka zikopa za tiana tambuzi pa manja ace ndi pakhosi pace posalala;

17. ndipo anapereka m'dzanja la mwana wace Yakobo cakudya cokoleraco, ndi mikate imene anaipanga.

18. Ndipo iye analowa kwa atate wace, nati, Atate wanga; iye anati, Ndine pano; ndani iwe mwana wanga?

19. Ndipo Yakobo anati kwa atate wace, Ndine Esau mwana wanu wamkuru; ndacita monga mwandiuza ine; ukanitu, khalani tsonga, idyani nyama yanga kuti moyo wanu undidalitse ine.

20. Ndipo Isake anati kwa mwana wace, Unaipeza msanga bwanji mwana wanga? Ndipo anati, Cifukwa kuti Yehova Mulungu wanu anandiyendetsa ine bwino.

21. Ndipo Isake anati kwa Yakobo, Sendera kuno, ndikuyambase mwana wanga, ngati ndiwe mwana wanga Esau ndithu, kapena wina.

22. Ndipo Yakobo anasendera kwa Isake atate wace, ndipo anamyambasa nati, Mau ndi mau a Yakobo, koma manja ndi manja a Esau.

23. Ndipo sanazindikira iye, cifukwa kuti manja ace anali aubweya, onga manja a Esau mkuru wace; ndipo anamdalitsa iye.

24. Ndipo anati, Kodi ndiwe mwana wanga weniweni Esau? ndipo anati, Ndine amene.

25. Ndipo iye anati, Usendere nayo kwa ine, ndidye nyama ya mwana wanga, kuti moyo wanga ukudalitse iwe. Ndipo anasendera nayo kwa iye, nadya iye; ndipo anamtengera vinyo, namwa iye.

26. Ndipo Isake atate wace anati kwa iye, Senderatu, undimpsompsone mwana wanga.

27. Ndipo anasendera nampsompsona; ndipo anamva kununkhira kwa zobvala zace, namdalitsa, nati,Taona, kununkhira kwa mwana wanga,Kufanana ndi kununkhira kwa munda anaudalitsa Yehova;

Werengani mutu wathunthu Genesis 27