Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 27:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo panali atakalamba Isake, ndi maso ace anali a khungu losaona nalo, anamuitana Esau mwana wace wamwamuna wamkuru, nati kwa iye, Mwana wanga; ndipo anati kwa iye, Ndine pano.

2. Ndipo anati, Taonatu, ndakalamba, sindidziwa tsiku la kufa kwanga:

3. tsopano tengatu zida zako ndi phodo lako ndi uta wako, numuke kuthengo kundisakira ine nyama;

4. nundikonzere ine cakudya cokolera conga comwe ndicikonda ine, nudze naco kwa ine kuti ndidzadye; kuti moyo wanga ukadalitse iwe ndisanafe.

5. Ndipo anamva Rebeka pamene Isake ananena ndi Esau mwana wace. Ndipo Esau ananka kuthengo kukasaka nyama ndi kubwera nayo.

6. Ndipo Rebeka ananena kwa Yakobo mwana wace, nati, Taona ndinamva atate wako alinkunena ndi Esau mkuru wako kuti,

7. Unditengere ine nyama, undikonzere ine cakudya cokolera, kuti ndidzadye, ndi kudalitsa iwe pamaso pa Yehova, ndisanafe.

8. Tsopanotu mwana wanga, tamvera mau anga monga momwe nditi ndikuuze iwe.

9. Pitatu kubusa, ukanditengere ine kumeneko tiana tiwiri tabwino ta mbuzi; ndikonzere nato cakudya cokolera ca atate wako conga comwe acikonda:

Werengani mutu wathunthu Genesis 27