Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 26:24-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Ndipo Yehova anamuonekera iye usiku womwewo, nati, Ine dine Mulungu wa Abrahamu atate wako; usaope, cifukwa kuti Ine ndiri ndi iwe, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kucurukitsa mbeu zako, cifukwa ca Abrahamu kapolo wanga.

25. Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, naitana dzina la Yehova, namanga hema wace kumeneko: ndi pamenepo anyamata a Isake anakumba citsime.

26. Ndipo ananka kwa iye Abimeleke kucokera ku Gerari, ndi Ahuzati bwenzi lace, ndi Fikoli, kazembe wa nkhondo yace.

27. Ndipo Isake anati kwa iwo, Mwandidzera cifukwa ciani, inu akundida ine, ndi kundicotsa kwanu?

28. Ndipo iwo anati, Kuona tinaona kuti Yehova ali ndi iwe; ndipo tinati, Tilumbiriranetu tonse awiri, ife ndi iwe, ticite pangano ndi iwe;

29. kuti usaticitire ife zoipa, pakuti sitidakhudza iwe, sitidakucirira kanthu koma kabwino ndiko, ndipo takulola umuke ndi mtendere; ndiwe tsopano wodalitsidwa ndi Yehova.

30. Ndipo anakonzera iwo madyerero, ndipo anadya namwa.

31. Ndipo analawira m'mamawa nalumbirirana wina ndi mnzace; ndipo Isake anawalola amuke, ndipo anauka kucokera kwa iye m'mtendere.

32. Ndipo panali tsiku lomwelo anyamata ace a Isake anadza namuuza iye za citsime cimene anakumba, nati kwa iye, Tapeza madzi.

33. Ndipo anacha dzina lace Seba, cifukwa cace dzina la mudziwo ndi Beereseba kufikira lero lino.

34. Pamene Esau anali wa zaka makumi anai, anakwatira Yuditi mwana wamkazi wa Beeri Mhiti, ndi Basemati mwana wamkazi wa Elone Mhiti:

35. ndipo iwo anapweteka mtima wa Isake ndi wa Rebeka.

Werengani mutu wathunthu Genesis 26