Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 26:23-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Ndipo anacoka kumeneko nakwera kunka ku Beereseba,

24. Ndipo Yehova anamuonekera iye usiku womwewo, nati, Ine dine Mulungu wa Abrahamu atate wako; usaope, cifukwa kuti Ine ndiri ndi iwe, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kucurukitsa mbeu zako, cifukwa ca Abrahamu kapolo wanga.

25. Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, naitana dzina la Yehova, namanga hema wace kumeneko: ndi pamenepo anyamata a Isake anakumba citsime.

26. Ndipo ananka kwa iye Abimeleke kucokera ku Gerari, ndi Ahuzati bwenzi lace, ndi Fikoli, kazembe wa nkhondo yace.

27. Ndipo Isake anati kwa iwo, Mwandidzera cifukwa ciani, inu akundida ine, ndi kundicotsa kwanu?

28. Ndipo iwo anati, Kuona tinaona kuti Yehova ali ndi iwe; ndipo tinati, Tilumbiriranetu tonse awiri, ife ndi iwe, ticite pangano ndi iwe;

Werengani mutu wathunthu Genesis 26