Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 26:12-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo Isake anabzala m'dzikomo, nalandira za makumi khumi caka cimeneco; ndipo Yehova anamdalitsa iye.

13. Ndipo anakula munthuyo, nakulakula kufikira kuti anakhala wamkurukuru:

14. ndipo anali ndi cuma ca nkhosa, ndi cuma ca zoweta, ndi banja lalikuru: ndipo Afilisti anamcitira iye nsanje.

15. Ndipo zitsime zonse anakumba anyamata a atate wace Afilisti anazitseka, nazikwirira ndi dothi.

16. Ndipo Abimeleke anati kwa Isake, Ucoke kwa ife cifukwa kuti iwe uti wamkuru wopambana ife.

17. Ndipo Isake anacoka kumeneko, namanga hema wace m'cigwa ca Gerari, nakhala kumeneko.

18. Ndipo Isake anafukulanso zitsime za madzi, anazikumba masiku a Abrahamu atate wace; cifukwa kuti Afilisti anazitseka atafa Abrahamu: ndipo anazicha maina monga maina omwe anazicha atate wace.

19. Ndipo anyamata a Isake anakumba m'cigwa, napeza kumeneko citsime ca madzi otumphuka.

20. Ndipo abusa a Gerari anakangana ndi abusa a Isake kuti, Madzi ndi athu; ndipo anacha dzina la citsimeco Eseke: cifukwa anakangana nave.

21. Ndipo anakumbanso citsime cina, ndipo anakangana naconso; nacha dzina lace Sitina.

22. Ndipo anacoka kumeneko nakumba citsime cina; koma sanakangana naco cimeneco; ndipo anacha dzina lace Rehoboti; ndipo anati, Cifukwa kuti tsopano Yehova anatipatsa ife malo, ndipo tidzabalana m'dziko muno.

Werengani mutu wathunthu Genesis 26