Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 25:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Abrahamu anatenga mkazi wina dzina lace Ketura.

2. Ndipo anambalira iye Zimerani ndi Yokesani ndi Medani, ndi Midyani, ndi Yisebaki, ndi Sua.

3. Ndipo Yokesani anabala Seba, ndi Dedani. Ana a Dedani ndi Aasuri, ndi Aletusi, ndi Aleumi.

4. Ana a Midyani: Efa, ndi Efere, ndi Hanoki, ndi Abida, ndi Elida. Onse amenewa ndi ana a Ketura.

5. Ndipo Abrahamu amwali anampatsa Isake zonse anali nazo.

6. Koma kwa ana a akazi ace ang'ono amene Abrahamu anali nao Abrahamu anapatsa mphatso, nawacotsa iwo kwa Isake mwana wace, akali ndi moyo, kuti anke kum'mawa, ku dziko la kum'mawa.

7. Masiku a zaka za moyo wace wa Abrahamu amene anakhala ndi moyo ndiwo zaka zana limodzi, kudza makumi asanu ndi limodzi, kudza khumi ndi zisanu.

8. Ndipo Abrahamu anamwalira, nafa m'ukalamba wace wabwino, nkhalamba ya zaka zambiri; natengedwa akhale ndi a mtundu wace.

9. Ndipo ana ace Isake ndi Ismayeli anamuika iye m'phanga la Makipela, m'munda wa Efroni mwana wace wa Zohari Mhiti, umene uli patsogolo pa Mamre;

10. munda umene anagula Abrahamu kwa ana a Heti: pamenepo anamuika Abrahamu ndi Sara mkazi wace.

11. Ndipo panali atafa Abrahamu, Mulungu anamdalitsa Isake mwana wace; ndipo Isake anakhala pa Beere-lahai-roi.

Werengani mutu wathunthu Genesis 25