Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 21:28-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Ndipo Abrahamu anapatula ana a nkhosa akazi asanu ndi awiri pa okha.

29. Ndipo Abimeleke anati kwa Abrahamu, Nanga ana a nkhosa akazi asanu ndi awiri amene wapatula pa okha?

30. Ndipo anati, Ana a nkhosa akazi asanu ndi awiriwa uwalandire pa dzanja langa, kuti akhale mboni zanga, kuti ndakumba ine citsime cimeneci.

31. Cifukwa cace anacha malowo Beereseba: cifukwa pamenepo analumbira onse awiri.

32. Ndipo anapangana pangano pa Beereseba: ndipo anauka Abimeleke ndi Fikolo kazembe wa-nkhondo yace, nabwera kunka ku dziko la Afilisti.

33. Ndipo Abrahamu ananka mtengo wabwemba pa Beereseba, naitanira pamenepo dzina la Yehova, Mulungu wa nthawi zonse.

34. Ndipo Abrahamu anakhala ngati mlendo masiku ambiri m'dziko la Afilisti.

Werengani mutu wathunthu Genesis 21