Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 20:13-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo panali pamene Mulungu anandiyendetsa ine kunyumba kwa atate wanga, ndinati kwa mkaziyo, Ici ndico cokoma mtima udzandicitire ine, konse kumene tidzafika ife, uzinena za ine, iye ndiye mlongo wanga.

14. Ndipo Abimeleke anatenga nkhosa ndi ng'ombe nd akapolo ndi adzakazi nampatsa Abrahamu, nambwezera iye Sara mkazi wace.

15. Ndipo Abimeleke anati, Taona dziko langa liri pamaso pako; kumene kuli kwabwino pamaso pako takhala kumeneko.

16. Kwa Sara ndipo anati, Taona, ndapatsa mlongo wako ndalama za siliva mazana khumi; taona, izo ndizo zoyeretsa maso za kwa onse amene ali ndi iwe: ndi pamaso pa onse ukhale wolungama.

17. Ndipo Abrahamu anapemphera Mulungu, ndipo Mulungu anaciritsa Abimeleke, ndi mkazi wace, ndi adzakazi ace; ndipo anabala ana.

18. Pakuti Yehova anatseketsa mimba yonse ya a m'nyumba ya Abimeleke, cifukwa ca Sara mkazi wace wa Abrahamu.

Werengani mutu wathunthu Genesis 20