Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 2:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo zinatha kupangidwa zakumwamba ndi dziko lapansi, ndi khamu lao lonse.

2. Tsiku lacisanu ndi ciwiri Mulungu anamariza nchito yonse anaipanga; ndipo anapuma tsiku lacisanu ndi ciwiri ku nchito yace yonse.

3. Mulungu ndipo anadalitsa tsiku lacisanu ndi ciwiri, naliyeretsa limenelo: cifukwa limenelo ada puma ku nchito yace yonse imene Mulungu anailenga ndi kupanga.

4. Imeneyo ndiyo mibadwo yao ya zakumwamba ndi dziko lapansi, pamene zinalengedwa, tsiku lomwe Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zakumwamba.

5. Ndi zomera zonse za m'munda zisanakhale m'dziko lapansi, ndiponso matherere onse a m'munda asanamere; cifukwa Yehova Mulungu sanabvumbitsire mvula pa dziko lapansi, ndipo panalibe munthu wakulima nthaka;

6. kama inakwera nkhungu yoturuka pa dziko lapansi, niithirira ponse pamwamba pa nthaka.

7. Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwace; munthuyo nakhala wamoyo.

8. Ndipo Yehova Mulungu anabzala m'munda ku Edene cakum'mawa; momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo.

9. Ndipo Yehova Mulungu anameretsa m'nthaka mitengo yonse yokoma m'maso ndi yabwino kudya; ndiponso mtengo wa moyo pakati pa mundapo, ndi mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa.

Werengani mutu wathunthu Genesis 2