Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 19:18-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo Loti anati kwa iwo, Iaitu, mfumu;

19. taonanitu, kapolo wanu anapeza ufulu pamaso panu, ndipo munakuza cifundo canu, cimene munandicitira ine, pakupulumutsa moyo wanga; ine sindikhoza kuthawira kuphiri kuti cingandipeze ine coipaco ndingafe:

20. taonanitu, mudzi uwu uli pafupi pothawirapo, ndipo uli wong'ono; ndithawiretu kumeneko, suli wong'ono nanga? ndipo ndidzakhala ndi moyo.

21. Ndipo anati kwa iye, Taona, ndikubvomereza iwe pamenepanso kuti sindidzaononga mudzi uwu umene wandiuza.

22. Fulumira, thawira kumeneko; pakuti sindithai kucita kanthu usadafike kumeneko. Cifukwa cace anacha dzina la mudziwo Zoari.

23. Ndipo dzuwa lidakwera pa dziko pamene Loti anafika ku Zoari.

24. Ndipo Yehova anabvumbitsa pa Sodomu ndi pa Gomora miyala ya sulfure ndi mota kuturuka kwa Mulungu kumwamba;

25. ndipo anaononga midziyo, ndi cigwa conse, ndi onse akukhala m'midzimo, ndi zimene zimera panthaka.

26. Koma mkazi wace anaceuka ali pambuyo pace pa Loti, nasanduka mwala wamcere.

27. Ndipo Abrahamu analawiram'mamawa kunka kumalo kumene anaima pamaso pa Yehova:

28. ndipo anayang'anira ku Sodomu ndi ku Gomora ndi ku dziko lonse la cigwa, ndipo anapenya, taonanitu, utsi wa dzikolo unakwera, monga utsi wa ng'anjo.

29. Ndipo panali pamene Mulungu anaononga midzi ya m'cigwa, Mulungu anakumbukira Abrahamu, naturutsa Loti pakati pa cionongeko, pamene anaononga midzi m'mene anakhalamo Loti.

30. Ndipo Loti anabwera kuturuka m'Zoari nakhala m'phiri ndi ana akazi awiri pamodzi naye: cifukwa anaopa kukhala m'Zoari, ndipo anakhata m'phanga, iye ndi ana ace akazi.

31. Woyamba ndipo anati kwa wamng'ono, Atate wathu akalamba, ndipo palibe pa dziko lapansi mwamona amene adzalowa kwa ife monga amacita pa dziko lonse lapansi:

32. tiyeni, timwetse atate vinyo, tidzagona naye, kuti tisunge mbeu za atate wathu.

33. Ndipo anamwetsa atate wao vinyo usiku womwewo; woyamba ndipo analowa nagona naye atate wace; ndipo sanadziwa pomwe anagona ndi pomwe anauka,

34. Ndipo panali m'mamawa, woyamba anati kwa wamng'ono, Taona, ndinagona ine ndi atate wanga usiku walero: timwetsenso iye usikunso: udzalowe nugone naye kuti tisunge mbeu za atate wathu.

35. Ndipo anamwetsa vinyo atate wao usiku womwenso; wamng'ono ndipo anauka nagona naye; ndipo iye sanadziwa pomwe anagona ndi pomwe anauka.

36. Ndipo ana akazi awiri a Loti anali ndi pakati pa atate wao.

37. Woyamba ndipo anabala mwana wamwamona, namcha dzina lace. Moabu; yemweyo ndi atate wa Amoabu kufikira lero.

Werengani mutu wathunthu Genesis 19