Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 19:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anadza ku Sodomu madzulo amithenga awiri; ndipo Loti anakhala pa cipata ca Sodomu, ndipo Loti anaona iwo, nauka kuti akakomane nao, ndipo anaweramitsa pansi nkhope yace.

2. Ndipo anati, Taonanitu, ambuye anga, tembenukanitu, kulowa m'nyumba mwa kapolo wanu, mugone usiku wonse, mutsuke mapazi anu, ndipo mudzalawira m'mawa kunka ulendo wanu. Ndipo anati, lai; koma tigone m'khwalalamu usiku wonse.

3. Ndipo anawaumiriza iwo ndithu: ndipo anapatukira kwa iye, nalowa m'nyumba mwace; ndipo anawakonzera iwo madyerero, naphika mikate yopanda cotupitsa, ndipo anadya,

4. Koma asanagone, anthu a m'mudzimo anthu a Sodomu, anazinga nyumba, anyamata ndi okalamba, anthu onse a m'mbali zonse;

5. ndipo anamuitana Loti, nati kwa iye, Ali kuti anthu amene anadza kwa iwe madzulo ano, utiturutsire iwo kuti tiwadziwe.

6. Ndipo Loti anaturukira kwa iwo pakhomo, natseka cambuyo pakhomo pace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 19