Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 18:7-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo Abrahamu anafulumira kunka kuzoweta, natenga kamwana ka ng'ombe kofewa ndi kabwino, napatsa mnyamata, ndipo anafulumira kuphika.

8. Ndipo anatenga mafuta amkaka, ndi mkaka, ndi kamwana ka ng'ombe kamene anaphika, naziika patsogolo pao; ndipo iye anaimirira iwo patsinde pa mtengo, ndipo anadya.

9. Ndipo anati kwa iye, Ali kuti Sara mkazi wako? Ndipo anati, Taonani m'hemamo.

10. Ndipo anati, Ndidzabwera kwa iwe ndithu pakufika nyengo yace; taonani Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna. Ndipo Sara anamva pakhomo pa hema amene anali pambuyo pace.

11. Koma Abrahamu ndi Sara anali okalamba, ana pitirira masiku ao; ndipo kunaleka kwa Sara konga kumacita ndi akazi;

12. ndipo Sara anaseka m'mtima mwace, nati, Kodi ndidzakhala ndi kukondwa ine nditakalamba, ndiponso mbuyanga ali wokalamba?

13. Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, Bwanji anaseka Sara, kuti, Kodi ndidzabala ine ndithu, ine amene ndakalamba?

14. Kodi ciripo cinthu comlaka Yehova? Pa nthawi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yace, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.

15. Koma Sara anakana, nati, Sindinasekai; cifukwa anaopa, Ndipo anati, lai; koma unaseka.

16. Ndipo anthuwo anauka kucokera kumeneko nayang'ana ku Sodomu; ndipo Abrahamu ananka nao kuwaperekeza.

17. Ndipo Yehova adati, Kodi ndidzabisira Abrahamu cimene ndicita?

18. Pakuti Abrahamu adzakhala ndithu wamkuru ndi wamphamvu, ndipo mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsika mwa iye?

19. Cifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ace ndi banja lace la pambuyo pace, kuti asunge njira ya Yehova, kucita cilungamo ndi ciweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu comwe anamnenera iye.

Werengani mutu wathunthu Genesis 18