Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 18:4-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. nditengetu madzi pang'ono, ndikusambitseni mapazi anu, mupumule pansi pa mtengo;

5. ndipo ndidzatenga cakudya pang'ono, nimutonthoze mitima yanu; mutatero mudzapitirira, cifukwa mwafika kwa kapolo wanu. Ndipo anati, Cita comweco monga momwe wanena.

6. Ndipo Abrahamu analowa msanga m'hema wace kwa Sara, nati, Konza msanga miyeso itatu ya ufa wosalala, nuumbe, nupange mikate.

7. Ndipo Abrahamu anafulumira kunka kuzoweta, natenga kamwana ka ng'ombe kofewa ndi kabwino, napatsa mnyamata, ndipo anafulumira kuphika.

8. Ndipo anatenga mafuta amkaka, ndi mkaka, ndi kamwana ka ng'ombe kamene anaphika, naziika patsogolo pao; ndipo iye anaimirira iwo patsinde pa mtengo, ndipo anadya.

9. Ndipo anati kwa iye, Ali kuti Sara mkazi wako? Ndipo anati, Taonani m'hemamo.

10. Ndipo anati, Ndidzabwera kwa iwe ndithu pakufika nyengo yace; taonani Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna. Ndipo Sara anamva pakhomo pa hema amene anali pambuyo pace.

11. Koma Abrahamu ndi Sara anali okalamba, ana pitirira masiku ao; ndipo kunaleka kwa Sara konga kumacita ndi akazi;

12. ndipo Sara anaseka m'mtima mwace, nati, Kodi ndidzakhala ndi kukondwa ine nditakalamba, ndiponso mbuyanga ali wokalamba?

Werengani mutu wathunthu Genesis 18