Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 15:10-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo anatenga iye zonse zimenezo, nazidula pakati, naika bandu popenyana ndi linzace: koma mbalame sanazidula.

11. Pamene miimba inatsikira panyama, Abramu anaingitsa iyo.

12. Ndipo linalinkulowa dzuwa, ndi tulo tatikuru tinamgwera Abramu: ndipo taonani, kuopsya kwa mdima waukuru kunamgwera iye.

13. Ndipo anati kwa Abramu, Dziwitsa ndithu kuti mbeu zako zidzakhala alendo m'dziko la eni, nizidzatumikira iwo, ndipo iwo adzasautsa izo zaka mazana anai;

14. ndiponso mtunduwo adzautumikira, Ine ndidzauweruza: ndiponso pambuyo pace adzaturuka ndi cuma cambiri.

15. Ndipo iwe udzanka kwa makolo ako m'mtendere; nudzaikidwa ndi ukalambawabwino.

16. Koma iwo adzabweranso kuno mbadwo wacinai: pakuti mphulupulu za Aamori sizinakwaniridwe.

17. Ndipo panali pamene litalowa dzuwa ndi kudza mdima, taonani, ng'anjo yofuka utsi ndi muuni wamoto wapita pakati pa mabanduwo.

18. Tsiku lomwelo Yehova anapangana cipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pa nyanja ya Aigupto kufikira pa nyanja yaikuru, nyanja ya Firate:

19. Akeni ndi Akenizi, Akadimoni, ndi Ahiti, ndi Aperezi, ndi Arefai, ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Agirigasi, ndi Ajebusi.

Werengani mutu wathunthu Genesis 15