Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 14:2-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. iwo anathira nkhondo pa Bera mfumu ya Sodomu, ndi pa Birisa, mfumu ya Gomora, ndi pa Sinabi mfumu ya Adima, ndi pa Semebere mfumu ya Ziboimu, ndi pa mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zoari).

3. Onse amenewo anadziphatikana pa cigwa ca Sidimu (pamenepo ndi pa nyanja yamcere).

4. Zaka khumi ndi ziwiri iwo anamtumikira Kedorelaomere, caka cakhumi ndi citatu anapanduka,

5. Caka cakhumi ndicinai ndipo anadza Kedorelaomere ndi mafumu amene anali naye, nawakantha Arefai m'Aseteroti-kamaimu, ndi Azuzi m'Hamu, ndi Aemi m'Savekiriataimu,

6. ndi Ahori pa phiri lao Seiri kufikira ku Eliparana, kumene kuli pacipululu.

Werengani mutu wathunthu Genesis 14