Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 1:9-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo anati Mulungu, Madzi a pansi pa kumwamba asonkhane pamodzi pa malo amodzi, uoneke mtunda: ndipo kunatero.

10. Ndipo Mulungu adaucha mtundawo Dziko lapansi; kusonkhana kwa madziko ndipo adaucha Nyanja: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.

11. Mulungu ndipo anati, Dziko lapansi limere maudzu, therere lobala mbeu, ndi mtengo wazipatso wakubala zipatso monga mwa mtundu wace, momwemo muli mbeu yace, pa dziko lapansi: ndipo kunatero.

12. Ndipo dziko lapansi linamera maudzu, therere lobala mbeu monga mwa mtundu wace, ndi mtengo wakubala zipatso, momwemo muli mbeu yace, monga mwa mtundu wace; ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.

13. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lacitatu.

14. Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pa thambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka;

Werengani mutu wathunthu Genesis 1