Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 1:4-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo anaona Mulungu kuti kuyerako kunali kwabino: ndipo Mulungu analekanitsa kuyera ndi mdima.

5. Ndipo Mulungu anacha kuyerako Usana, ndi mdimawo anaucha Usiku. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku loyamba.

6. Ndipo anati Mulungu, Pakhale thambo pakati pa madzi, lilekanitse madzi ndi madzi.

7. Ndipo Mulungu anapanga thambo, nalekanitsa madzi anali pansi pa thambolo ndi madzi analf pamwamba pa thambolo: ndipo kunatero.

8. Ndipo Mulungu analicha thambolo Kumwamba. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku laciwiri.

9. Ndipo anati Mulungu, Madzi a pansi pa kumwamba asonkhane pamodzi pa malo amodzi, uoneke mtunda: ndipo kunatero.

10. Ndipo Mulungu adaucha mtundawo Dziko lapansi; kusonkhana kwa madziko ndipo adaucha Nyanja: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.

11. Mulungu ndipo anati, Dziko lapansi limere maudzu, therere lobala mbeu, ndi mtengo wazipatso wakubala zipatso monga mwa mtundu wace, momwemo muli mbeu yace, pa dziko lapansi: ndipo kunatero.

12. Ndipo dziko lapansi linamera maudzu, therere lobala mbeu monga mwa mtundu wace, ndi mtengo wakubala zipatso, momwemo muli mbeu yace, monga mwa mtundu wace; ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.

13. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lacitatu.

14. Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pa thambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka;

15. zikhale zounikira m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire pa dziko lapansi; ndipo kunatero.

16. Ndipo Mulungu anapanga zounikira zazikuru ziwiri; counikira cacikuru cakulamulira usana, counikira cacing'ono cakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe.

Werengani mutu wathunthu Genesis 1