Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 1:14-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pa thambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka;

15. zikhale zounikira m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire pa dziko lapansi; ndipo kunatero.

16. Ndipo Mulungu anapanga zounikira zazikuru ziwiri; counikira cacikuru cakulamulira usana, counikira cacing'ono cakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe.

17. Mulungu ndipo adaika zimenezo m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire pa dziko lapansi,

18. nizilamulire usana ndi usiku, nizilekanitse kuyera ndi mdima: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabino.

19. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lacinai.

Werengani mutu wathunthu Genesis 1