Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 9:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo Iye anapfuula m'makutu mwanga ndi mau akuru, ndi kuti, Asendere oyang'anira mudzi, ali yense ndi cida cace coonongera m'dzanja lace.

2. Ndipo taonani, anadza amuna asanu ndi mmodzi, odzera njira ya cipata ca kumtunda coloza kumpoto, ali yense ndi cida cace cophera m'dzanja lace; ndi munthu mmodzi pakati pao wobvala bafuta, ndi zolembera nazo m'cuuno mwace. Ndipo analowa, naima m'mphepete mwa guwa la nsembe lamkuwa.

3. Ndipo ulemerero wa Mulungu wa Israyeli unakwera kucoka pakerubi, pamene unakhalira kumka ku ciunda ca nyumba, naitana munthu wobvala bafutayo wokhala ndi zolembera nazo m'cuuno mwace.

4. Ndipo Yehova ananena naye, Pita pakati pa mudzi, pakati pa Yerusalemu, nulembe cizindikilo pa mphumi zao za anthu akuusa moyo ndi kulira cifukwa ca zonyansa zonse zicitidwa pakati pace.

5. Nati kwa enawo, nditikumva ine, Pitani pakati pa mudzi kumtsata iye, ndi kukantha; maso anu asalekerere, musacite cifundo;

6. iphanitu nkhalamba, mnyamata ndi namwali, makanda, ndi akazi; koma musayandikira munthu ali yense ali naco cizindikilo, ndipo muyambe pa malo anga opatulika, Pamenepo anayamba ndi akuluwo anali pakhomo pa nyumba.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 9