Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 8:16-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo anadza nane ku bwalo lam'kati la nyumba ya Yehova, ndipo taonani, pa khomo la Kacisi wa Yehova, pakati pa khonde lace ndi guwa la nsembe, panali amuna ngati makumi awiri mphambu asanu akufulatira, ku Kacisi wa Yehova, ndi kuyang'ana kum'mawa; napembedza dzuwa kum'mawa.

17. Ndipo anati kwa ine, Waciona ici, wobadwa ndi munthu iwe? Cinthu copepuka ici kodi ndi nyumba ya Yuda, kuti acite zonyansa azicita kunozi? pakuti anadzaza dziko ndi ciwawa, nabwereranso kuutsa mkwiyo wanga, ndipo taonani, aika nthambi kumphuno kwao.

18. Cifukwa cace Inenso ndidzacita mwaukali; diso langa silidzalekerera, osawacitira cifundo Ine; ndipo cinkana apfuula m'makutu mwanga ndi mau akulu, koma sindidzawamvera ine.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 8