Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 8:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali caka cacisanu ndi cimodzi, mwezi wacisanu ndi cimodzi, tsiku lacisanu la mweziwo, pokhala ine m'nyumba mwanga, akulu a Yuda omwe analikukhala pamaso panga, dzanja la Yehova Mulungu linandigwera komweko.

2. Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, cifaniziro ca maonekedwe a moto; kuyambira maonekedwe a m'cuuno mwace ndi kunsi kwace, moto; ndi kuyambira m'cuuno mwace ndi kumwamba kwace, monga maonekedwe a ceza, ngan citsulo cakupsa.

3. Ndipo anatambasula conga dzanja, nandigwira tsitsi la pamutu panga; ndipo mzimu unandilengetsa pakati pa dziko ndi thambo, numuka nane m'masomphenya a Mulungu ku Yerusalemu, ku citseko ca cipata ca bwalo la m'katimo loloza kumpoto, kumene kunali mpando wa fano la nsanje locititsa nsanje.

4. Ndipo taonani, pomwepo panali ulemerero wa Mulungu wa lsrayeli, monga mwa maonekedwe ndinawaona ku cidikha cija.

5. Pamenepo ananena ndi ine, Wobadwa ndi munthu iwe, kweza maso ako ku njira yoloza kumpoto. Ndipo ndinakweza maso anga ku njira yoloza kumpoto, ndipo taonani, kumpoto kwa cipata ca guwa la nsembe fano ili la nsanje polowera pace.

6. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, uona kodi izi alikuzicita? zonyansa zazikulu nyumba ya Israyeli irikuzicita kuno, kuti ndicoke kutali kwa malo anga opatulika? Koma udzaonanso zonyansa zina zoposa.

7. Ndipo anadza nane ku cipata ca kubwalo, ndipo popenya ine, taonani, pobooka palinga.

8. Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, booletsa kulinga; ndipo nditabooletsa palinga, ndinaona khomo.

9. Ndipo anati kwa ine, Lowa, kapenye zonyansa zoipa alikuzicita komweko.

10. M'mwemo ndinalowa ndi kupenya, ndipo taonani, maonekedwe ali onse a zokwawa, ndi zirombo zonyansa, ndi mafano onse a nyumba ya Israyeli, zolembedwa pakhoma pozungulira ponse.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 8