Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 7:5-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Atero Yehova Mulungu, Coipa, coipa ca pa cokha, taona cirinkudza.

6. Kutha kwafika, kwafika kutha, kwakugalamukira, taona kwafika.

7. Tsoka lako lakufikira, nzika iwe, yafika nthawi, tsiku liri pafupi, ndilo laphokoso, si lakupfuula mokondwera kumapiri,

8. Katsala kamphindi, ndipo ndidzakutsanulira ukali wanga, ndi kukukwaniritsira mkwiyo wanga, ndi kukuweruza monga mwa njira zako, ndipo ndidzakubwezera zonyansa zako zonse.

9. Ndipo diso langa silidzalekerera, wosacita cifundo Ine, ndidzakubwezera monga mwa njira zako, ndi zonyansa zako zidzakhala pakati pako; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova wakukantha.

10. Taona, tsikuli, taona, lafika; tsoka lako laturuka, ndodo yaphuka mphundu za maluwa, kudzitama kwaphuka.

11. Ciwawa cauka cikhale ndodo ya coipa; sadzawatsalira ndi mmodzi yense, kapena wa unyinji wao, kapena wa cuma cao; sipadzakhalanso kuwalira maliro.

12. Yafika nthawi, layandikira tsikulo, wogula asakondwere, ndi wogulitsa asamve cisoni; pakuti mkwiyo ukhalira unyinji wao wense.

13. Pakuti wogulitsa sadzabwera ku cogulitsaco, cinkana akali ndi moyo, popeza masomphenyawo akunena unyinji wace wonse sadzapita pacabe, ndipo palibe mmodzi adzalimbitsa moyo wace m'mphulupulu yace.

14. Aomba lipenga, nakonzeratu zonse, koma palibe womuka kunkhondo; pakuti mkwiyo wanga ukhalira unyinji wace wonse.

15. Kunja kuli lupanga, ndi m'katimo muli mliri ndi njala; wokhala kuthenso adzafa ndi lupanga, ndi wokhala m'mudziyo njala ndi mliri zidzamutha.

16. Ndipo akupulumuka mwa iwo adzapulumuka, koma adzakhala kumapiri ngati njiwa za kuzigwa, onse akubuula, ali yense m'mphulupulu zace.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 7