Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 7:23-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Sula unyolo, popeza dziko ladzala ndi mirandu yamwazi, ndi mudzi wadzala ndi ciwawa.

24. Cifukwa cace ndidzabwera nao amitundu oipitsitsa, ndipo iwo adzalandira nyumba zao ngati colowa, ndidzaleketsanso kudzikuza kwa amphamvu, kuti adetsedwe malo ao opatulika.

25. Cionongeko cirinkudza, adzafunafuna mtendere, koma palibe.

26. Lidzafika tsoka lotsatana-tsatana, kudzakhalanso mbiri yotsatana-tsatana, ndipo adzafunafuna masomphenya a mneneri, koma malamulo adzatayikira wansembe, uphungu ndi kutayikira akulu.

27. Mfumu idzalira maliro, ndi kalonga adzabvala cipasuko, ndi manja a anthu a m'dziko adzanjenjemera, Ndidzawacitira monga mwa njira zao, ndi kuwaweruza monga mwa maweruzo ao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 7