Pamenepo anaturuka nane njira ya ku cipata ca kumpoto, nazungulira nane njira yakunja kumka ku cipata cakunja, njira ya ku cipata coloza kum'mawa; ndipo taonani, panaturuka madzi pa mbali ya kulamanja.