Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 42:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo anaturuka nane kumka ku bwalo la kunja, njira ya kumpoto; nalowa nane ku nyumba yazipinda idali pandunji pa mpatawo, ndi pandunji pa nyumbayo inaloza kumpoto.

2. Cakuno ca m'litali mwace mwa mikono zana limodzi kunali khomo la kumpoto, ndi kupingasa kwace mikono makumi asanu.

3. Pandunji pa mikono makumi awiri a bwalo lam'kati, ndi pandunji pa moyalamo mwa miyala, mwa bwalo lakunja, panali khonde lam'mwamba, lokomana ndi khonde linzace losanjikika paciwiri.

4. Ndi kukhomo kwa zipinda anakonza poyendapo, kupingasa kwace mikono khumi m'kati mwace, njira ya mikono zana limodzi, ndi makomo ao analoza kumpoto.

5. Ndipo zipinda zapamwamba zinacepa, pakuti makonde am'mwamba analanda pamenepo, cifukwa cace zinacepa koposa zapansi ndi zapakati m'nyumba yazipinda.

6. Pakuti zinasanjikizana pawiri, ndipo zinalibe nsanamira ngati nsanamira za kumabwalo; cifukwa cace zam'mwambazo zinacepa koposa zakunsi ndi zapakati kuyambira pansi.

7. Ndipo linga linali kunialo, loli'ngana ndi nyumba yazipinda, kuloza ku bwalo lakunja, popenyana ndi nyumba yazipinda, m'litali mwace munali mikono makumi asanu.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 42