Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 41:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anadza nane ku Kacisi, nayesa nsanamira zace, kupingasa kwace mikono isanu ndi umodzi cakuno, ndi mikono isanu ndi umodzi cauko, ndiko kupingasa kwa cihema cija.

2. Ndi kupingasa kwa khomo mikono khumi; ndi mbali za khomo mikono isanu cakuno, ndi mikono isanu cauko; nayesa malo opatulika, m'litali mwace mikono makumi anai, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri.

3. Nalowa m'katimo, nayesa mphuthu za pakhomo mikono iwiri, ndi msinkhu wa khomo mikono isanu ndi umodzi, ndi kupingasa kwa khomo mikono isanu ndi iwiri.

4. Anayesanso m'kati mwa Kacisi m'tsogolomo, m'litali mwace mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri; ndipo anati kwa ine, Umo m'mopatulikitsa.

5. Pamenepo anayesa khoma la nyumba, kucindikira kwace mikono isanu ndi umodzi, ndi kupingasa kwace kwa zipinda za m'mphepete mikono inai, pozungulira pace ponse pa kacisi.

6. Ndipo zipinda za m'mphepete zinasanjikizana cina pa cinzace; zinatero makumi atatu mizere yonse itatu, nizinalowa ku khoma locirikiza zipinda za m'mphepete pozungulirapo, zisanjikike pamenepo; pakuti sizinagwiridwa ndi khoma la nyumba.

7. Ndipo zipinda za m'mphepete zinakula m'kupingasa kwao, pozinga nyumba m'kukwera kwao; pakuti nyumba inazingika mokwerakwera pozungulira pace pa nyumba; motero kupingasa kwace kwa nyumba kunakula kumwamba kwace, momwemonso anakwera kuyambira cipinda cakunsi, kupita capakati, kufikira cam'mwamba.

8. Ndinaonanso kuti kunyumba kunali ciunda pozungulira pace; maziko a zipinda za m'mphepete anafikira muyeso wa bango la mikono isanu ndi umodzi yaikuru.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 41